English items | Chichewa items |
---|---|
Physical exercise contributes to good mental health | Kuchita masewela olimbitsa thupi kumathandiza kuti munthu akhale ndi umoyo wabwino wa ubongo |
A person with depression feels very miserable. | Muntha odwala matenda a nkhawa amakhala osakondwa. |
People with schizophrenia usually have delusions (e.g., they may believe they are constantly being followed and observed). | Anthu odwala matenda a mubongo ngati ‘schizophrenia’ nthawi zambili amaona zinthu zomwe palibe (mwachitsanzo, atha kukhulupilila kuti wina wake akuwasatila kapena akuwalonda) |
If I had a mental disorder I would seek my relatives’ help. | Nditakhala ndi vuto / nthenda ya mubongo, nditha kupempha thandizo kwa achibale |
If someone close to me had a mental disorder, I would encourage her/him to look for a psychologist | M’bale wanga kapena nzanga atakhala ndi nthenda ya mubongo, nditha kumulimbikitsa kuti apeze katswiri wa maganizidwe / mubongo |
Mental disorders don’t affect people’s behaviours. | Matenda a mubongo sakhuzana ndi makhalidwe a`wanthu |
Sleeping well contributes to good mental health. | Kugona mokwanila kumathandiza kuti munthu akhale ndi umoyo wabwino wa ubongo. |
If I had a mental disorder, I would seek a psychologist’s help. | Nditakhala ndi nthenda ya mubongo, nditha kufufuza thandizo kwa katswiri wa maganizidwe / mubongo |
A person with anxiety disorder may panic in situations that she/he fears. | Munthu odwala matenda a nkhawa, atha kukhala ndi mantha opitilila miyezo zinthu zomwe amaopa zikamachitika |
People with mental disorders belong to low-income families. | Anthu omwe ali ndi matenda a mubongo amachokela m’mabanja a ndalama zochepa |
If someone close to me had a mental disorder, I would listen to her/him without judging or criticizing. | M’bale wanga kapena nzanga atakhala ndi nthenda ya mubongo, ndingathe kumumvela opanda kumuweluza kapena kumunyogodola |
Alcohol use may cause mental disorders. | Kumwa mowa kumatha kuyambitsa matenda a mubongo |
Mental disorders don’t affect people’s feelings. | Matenda a mubongo sakhudzana ndi m’mene anthu amamvelela muthupi |
The sooner the mental disorders are identified and treated, the better | Matenda a mubongo akadziwika ndi kuchilitsidwa msanga, zinthu zimakhala bwino |
Only adults have mental disorders. | Anthu akuluakulu okha ndi omwe amadwala matenda a mubongo |
Changes in brain function may lead to the onset of mental disorders | Kusintha kwa magwiridwe antchito a mubongo kutha kuyambitsa nthenda za mubongo |
If someone close to me had a mental disorder, I would encourage her/him to see a psychiatrist. | M’bale wanga kapena nzanga atakhala ndi nthenda ya mubongo, nditha kumulimbikitsa kuti akaonane ndi katswiri wa zamisala |
If I had a mental disorder I would seek for my friends’ help. | Nditakhala ndi nthenda ya mubongo, nditha kufufuza thandizo kwa anzanga |
A balanced diet contributes to good mental health. | Kudya moyenela kumathandizila kuti munthu akhale ndi thanzi labwino mubongo |
One of the symptoms of depression is the loss of interest or pleasure in most things. | Chimodzi mwazizindikilo zakukhumudwa ndikusakhala ndi chidwi kapena chisangalalo m’zinthu zambiri |
If someone close to me had a mental disorder, I could not be of any assistance | M’bale wanga kapena nzanga atakhala ndi nthenda ya mubongo, sindingathe kumuthandiza. |
The symptom’s length is one of the important criteria for the diagnosis of a mental disorder | Nthawi yimene zimatenga kuyeza zizindikilo za matenda a mubongo /misala, ndichinthu chofunika kwambili |
Depression is not a true mental disorder. | Matenda okhumudwa si vuto lenileni ya mubongo |
Drug addiction may cause mental disorders. | Kuledzela ndi kusuta kwambili kutha kuyambitsa matenda a mubongo |
Mental disorders affect people’s thoughts | Matenda a mubongo amakhudza kuganiza kwa anthu |
Doing something enjoyable contributes to a good mental health | Kuchita zinthu zosangalatsa kumathandiza kukhala ndi umoyo wabwino wa ubongo |
A person with schizophrenia may see and hear things that nobody else sees and hears. | Munthu odwala ‘schizophrenia’ amatha kuwona ndikumva zinthu zomwe wina saziwona kapena kuzimva. |
Highly stressful situations may cause mental disorders. | Zinthu zopatsa nkhawa kapena zovuta kwambili zimatha kuyambitsa matenda a mubongo. |
If I had a mental disorder, I would seek for a psychiatrist’s help. | Nditakhala ndi matenda a mubongo, nditha kupempha thandizo kwa katswiri wa zamisala |